Menu

MASALIMO 20

BIB

1 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze. 2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni. 3 Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza. Sela 4 Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike. 5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse. 6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja. 7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu. 8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa, koma ife timadzuka ndi kuyima chilili. 9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate