Menu

MASALIMO 8

BIB

1 Inu Yehova Ambuye athu, dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi! Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu mʼmayiko onse akumwamba. 2 Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda, Inu mwakhazikitsa mphamvu chifukwa cha adani anu, kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa. 3 Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake, 4 munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira, ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye? 5 Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu. 6 Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu; munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake; 7 nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi ndi nyama zakuthengo, 8 mbalame zamlengalenga ndi nsomba zamʼnyanja zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja. 9 Inu Yehova, Ambuye athu, dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Everything we make is available for free because of a generous community of supporters.

Donate